Hosea 7

1Pamene ndichiritsa Israeli,
machimo a Efereimu amaonekera poyera
ndiponso milandu ya Samariya sibisika.
Iwo amachita zachinyengo,
mbala zimathyola nyumba,
achifwamba amalanda anthu katundu mʼmisewu.
2Koma sazindikira kuti Ine
ndimakumbukira zoyipa zawo zonse.
Azunguliridwa ndi zolakwa zawo;
ndipo sizichoka mʼmaso mwanga.

3“Anthuwa amasangalatsa mfumu ndi zoyipa zawozo,
akalonga amasekerera mabodza awo.
4Onsewa ndi anthu azigololo,
otentha ngati moto wa mu uvuni,
umene wophika buledi sasonkhezera
kuyambira pamene akukanda buledi mpaka atafufuma.
5Pa tsiku la chikondwerero cha mfumu yathu
akalonga amaledzera ndi vinyo,
ndipo amalowa mʼgulu la anthu achipongwe.
6Mitima yawo ili ngati uvuni;
amayandikira Mulungu mwachiwembu.
Ukali wawo umanyeka usiku wonse,
mmawa umayaka ngati malawi a moto.
7Onsewa ndi otentha ngati uvuni,
amapha olamulira awo.
Mafumu awo onse amagwa,
ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amandiyitana Ine.

8“Efereimu wasakanikirana ndi mitundu ya anthu ena;
Efereimu ndi buledi amene wapsa mbali imodzi.
9Alendo atha mphamvu zake,
koma iye sakuzindikira.
Tsitsi lake layamba imvi
koma iye sakudziwa.
10Kunyada kwake Israeli kukumutsutsa,
koma pa zonsezi
iye sakubwerera kwa Yehova Mulungu wake
kapena kumufunafuna.

11“Efereimu ali ngati nkhunda
yopusa yopanda nzeru.
Amayitana Igupto
namapita ku Asiriya.
12Akamadzapita, ndidzawakola ndi ukonde wanga;
ndidzawagwetsa pansi ngati mbalame zamumlengalenga.
Ndikadzamva kuti asonkhana pamodzi
ndidzawakola.
13Tsoka kwa iwo,
chifukwa andisiya Ine!
Chiwonongeko kwa iwo,
chifukwa andiwukira!
Ndimafunitsitsa kuwapulumutsa
koma amayankhula za Ine monama.
14Iwo salirira kwa Ine kuchokera pansi pa mtima,
koma amalira mofuwula ali pa bedi pawo.
Amadzichekacheka chifukwa chofuna tirigu ndi vinyo watsopano,
koma amandifulatira.
15Ine ndinawaphunzitsa ndikuwalimbitsa,
koma amandikonzera chiwembu.
16Iwo satembenukira kwa Wammwambamwamba;
ali ngati uta woonongeka.
Atsogoleri awo adzaphedwa ndi lupanga
chifukwa cha mawu awo achipongwe.
Motero iwo adzasekedwa
mʼdziko la Igupto.
Copyright information for NyaCCL